Luka 7:11 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumzinda, dzina lake Naini; ndipo ophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumudzi, dzina lake Naini; ndipo ophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Yesu adapita ku mudzi wina, dzina lake Naini. Ophunzira ake pamodzi ndi anthu ena ambirimbiri adatsagana naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. |
Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.