ndipo anatulutsa khwangwala, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi padziko lapansi.
Genesis 8:8 - Buku Lopatulika Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba padziko lapansi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Nowa adatulutsa nkhunda kuti ikaone ngati madzi aphwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. |
ndipo anatulutsa khwangwala, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi padziko lapansi.
koma njiwayo siinapeze popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo padziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo.
Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola, maso ako akunga a nkhunda.
Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka, ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako; pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.