Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake.
Genesis 26:19 - Buku Lopatulika Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Antchito a Isaki adakumba chitsime m'chigwa, napezamo madzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Antchito a Isake anakumba mʼchigwamo ndipo anapezamo kasupe wa madzi. |
Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake.
Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye.
Ndiwe kasupe wa m'minda, chitsime cha madzi amoyo, ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni.
Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.