Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife.
Genesis 26:17 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki anachoka kumeneko, namanga hema wake m'chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki anachoka kumeneko, namanga hema wake m'chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Isaki adachoka nakamanga mahema m'chigwa cha Gerari nakhazikikako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Isake anachokako kumeneko nakakhala ku chigwa cha Gerari kumene anakhazikikako. |
Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife.
Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake.