Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Genesis 23:1 - Buku Lopatulika Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sara adakhala ndi moyo zaka 127, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sara anakhala ndi moyo zaka 127. |
Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Ndipo mkazi wake wamng'ono, dzina lake Reuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka.
Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.
Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake.