Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.
Genesis 22:13 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu atayang'ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m'ziyangoyango. Adapita kukaigwira, naipha ngati nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. |
Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.
Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.