Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
Genesis 20:8 - Buku Lopatulika Ndipo Abimeleki analawira m'mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abimeleki analawira m'mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abimeleki adaitana antchito ake onse naŵauza zonsezi, ndipo anthuwo adachita mantha kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmamawa mwake Abimeleki anayitanitsa akuluakulu ake onse, ndipo atawafotokozera zimene zinachitika, iwo aja anachita mantha kwambiri. |
Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.