Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Genesis 1:15 - Buku Lopatulika Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi: ndipo kunatero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.” |
Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.
Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero.