Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima padziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika.
Eksodo 9:22 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala padziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse zakuthengo, m'dziko la Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m'dziko la Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba, ndipo matalala adzagwa pa anthu, pa nyama, ndi pa zomera zonse zam'minda, m'dziko lonse la Ejipito.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti matalala agwe pa dziko lonse la Igupto, pa munthu aliyense, pa ziweto ndi pa zonse zomera mʼminda ya Igupto.” |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima padziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, pamtsinje, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule padziko la Ejipito.
Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.
Ndipo anatsika kumwamba matalala aakulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.