Eksodo 9:20 - Buku Lopatulika Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nduna zina za Farao zidachita mantha chifukwa cha mau amene adanena Chauta, ndipo zidatsekera akapolo ao m'nyumba pamodzi ndi zoŵeta zao zomwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nduna za Farao zinachita mantha ndi mawu a Yehova, ndipo zinalowetsa antchito awo ndi ziweto zawo mʼnyumba. |
Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za mu Ejipito; koma sichinafe chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.
Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.