Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;
Eksodo 8:13 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nafa achulewo kuchokera m'zinyumba, ndi m'mabwalo, ndi m'minda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nafa achulewo kuchokera m'zinyumba, ndi m'mabwalo, ndi m'minda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Motero achule onse aja amene adaali m'nyumba, pa bwalo ndi m'minda momwe, adafa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha. Achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anafa |
Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;
Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'mtsinje mokha.
Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao.