Eksodo 5:15 - Buku Lopatulika Pamenepo akapitao a ana a Israele anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo akapitao a ana a Israele anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono akapitao achiisraele aja adapita kwa Farao kukadandaula kuti, “Pepani amfumu, kaya chifukwa chiyani mwatichita zotere ife atumiki anu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja anapita kukadandaula kwa Farao kuti, “Chifukwa chiyani mwachitira antchito anu zotere? |
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.
Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsirize bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?
Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.