Eksodo 39:25 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapanganso timabelu ta golide wabwino kwambiri, mopakiza pakati pa makangazawo, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo. |
Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.