momwemonso pa mbali ina: pa mbali ino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu.
Eksodo 38:16 - Buku Lopatulika Nsalu zotchingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nsalu zochingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsalu zonse zochinga kuzungulira bwalolo zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Katani yonse yotchinga kuzungulira chihema inali yofewa, yosalala ndi yolukidwa bwino. |
momwemonso pa mbali ina: pa mbali ino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu.
Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.