ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Eksodo 38:10 - Buku Lopatulika nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsanamira zake makumi aŵiri, pamodzi ndi masinde ake makumi aŵiri, zonsezo zinali zamkuŵa, koma ngoŵe za pa nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zinali zasiliva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapanganso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. |
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ake makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.
Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;