Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono.
Eksodo 32:18 - Buku Lopatulika Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa ogonjetsa, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa olakika, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Mose adati, “Phokoso limenelo silikumveka ngati phokoso la opambana pa nkhondo, kapenanso kulira kwa ogonjetsedwa. Ndikumva phokoso la kuimba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anayankha kuti, “Phokoso limeneli sindikulimva ngati phokoso la opambana nkhondo, kapena kulira kwa ongonjetsedwa pa nkhondo. Koma ndikulimva ngati phokoso la anthu amene akuyimba.” |
Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono.
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.
Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.