Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa.
Eksodo 30:2 - Buku Lopatulika Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zituluke m'mwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zituluke m'mwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Likhale lalibanda, kutalika kwake masentimita 46, muufupi mwake likhalenso masentimita 46, ndipo msinkhu wake ukhale wa masentimita 91. Nyanga zake zipangidwire kumodzi ndi guwalo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. |
Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa.
Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.
Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.
Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu,