Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'onopang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo.
Eksodo 23:30 - Buku Lopatulika Ndidzawaingitsa pang'onopang'ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzawaingitsa pang'onopang'ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndidzaŵapirikitsa pang'onopang'ono, mpaka mutabala ana ambiri amene angathe kutenga dzikolo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzawathamangitsa pangʼonopangʼono mpaka inu mutachuluka kokwanira mwakuti nʼkutenga dzikolo. |
Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'onopang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo.
nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.
Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale cholowa cha mafuko anu, kuyambira ku Yordani, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa.
Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapirikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwachotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale cholowa chanu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.
Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.