Eksodo 21:23 - Buku Lopatulika Koma ngati kupweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma maiyo akampweteka, chilango chake chidzakhala chotere: moyo kulipa moyo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo, |
kuthyola kulipa kuthyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anachitira munthu chilema, momwemo amchitire iye.
Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.
Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.