Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
Eksodo 2:9 - Buku Lopatulika Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mwana wa Farao uja adauza maiyo kuti, “Mtengeni mwanayu, mukandilerere, ine ndidzakulipirani.” Motero mai uja adamtenga mwanayo, nakamlera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wa Farao anati, “Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani.” Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera. |
Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo.