Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Eksodo 2:7 - Buku Lopatulika Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mlongo wake wa mwanayo adafunsa kuti, “Bwanji ndikakuitanireni mai wachihebri woti akakulerereni mwanayu?” Mwana wa Farao uja adayankha kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, “Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?” |
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.
Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo.
Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.
Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi mu Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.