Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.
Eksodo 2:13 - Buku Lopatulika M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikumenyana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake atabweranso, adaona kuti Ahebri aŵiri akumenyana. Mose adafunsa wolakwayo kuti, “Chifukwa chiyani ukumumenya mnzako?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmawa mwake Mose anapita ndipo anaona anthu awiri a Chihebri akumenyana. Iye anafunsa amene anali wolakwa kuti, “Chifukwa chiyani ukumenya Mhebri mnzako?” |
Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.