Eksodo 18:18 - Buku Lopatulika Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mudzafooka msanga, pamodzi ndi anthu muli nawoŵa. Ntchito imeneyi njaikulu kuposa mphamvu zanu, ndipo simungaithe nokha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. |
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.