Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m'dziko la Ejipito;
Eksodo 16:5 - Buku Lopatulika Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pokonza chimene adatola adzapeza kuti nchokwanira masiku aŵiri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.” |
Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m'dziko la Ejipito;