Eksodo 15:19 - Buku Lopatulika Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene akavalo a Farao, pamodzi ndi magaleta ndi okwerapo ake omwe, adaloŵa m'nyanja, Chauta adaŵabweza madziwo, ndipo adamiza onsewo. Koma Aisraele adayenda pouma m'kati mwa nyanjayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma. |
amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.
Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.
Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordani pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anachitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka;