Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.
Eksodo 12:20 - Buku Lopatulika Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musadye chilichonse chofufumitsa, ndipo ku nyumba zanu zonse muzidzangodya buledi wosafufumitsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musadye chilichonse chokhala ndi yisiti. Kulikonse kumene mukukhala, muyenera kudya buledi wopanda yisiti.” |
Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.
Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.
Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa.
Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.