koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.
Danieli 6:24 - Buku Lopatulika Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse. |
koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.
koma pofika mlanduwo kwa mfumu, iye adalamula polemba kalata kuti chiwembu choipa cha Hamani adachipangira Ayuda chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana ake aamuna apachikidwe pamtengo.
Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.
Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.
Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego.
Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.