Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.
Danieli 6:21 - Buku Lopatulika Pamenepo Daniele anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Daniele anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Danieli anayankha kuti, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! |
Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.
Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu mu Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake.
Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, tulukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedenego, anatuluka m'kati mwa moto.
Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire.