Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Danieli 4:11 - Buku Lopatulika Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtengowo unakula ndi kulimba ndipo msonga yake inafika mpaka mlengalenga; umaonekera pa dziko lonse lapansi. |
Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.
Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya.
Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse yakuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu.
Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.
Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, mizinda yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,