Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 3:21 - Buku Lopatulika

Pamenepo amuna awa anamangidwa ali chivalire zofunda zao, malaya ao, ndi nduwira zao, ndi zovala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo amuna awa anamangidwa ali chivalire zofunda zao, malaya ao, ndi nduwira zao, ndi zovala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto.

Onani mutuwo



Danieli 3:21
6 Mawu Ofanana  

Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.


ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali mu Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaotcha m'moto;


Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lake la nkhondo amange Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto.


Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zofunda zao zosasandulika, fungo lomwe lamoto losawaomba.


ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.


ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.