Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 3:2 - Buku Lopatulika

Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwere kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwera kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija.

Onani mutuwo



Danieli 3:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.


Mkulu akamvera chinyengo, atumiki ake onse ali oipa.


Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zofunda zao zosasandulika, fungo lomwe lamoto losawaomba.


Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara.


popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.


amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.


Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikulu, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samisoni mdani wathu m'dzanja lathu.