Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Danieli 11:37 - Buku Lopatulika Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena chokhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena choikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi, sidzachitiranso ulemu mulungu aliyense, koma idzadzikweza yokha pamwamba pa onse. |
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.
Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikuchotsera chokonda maso ako ndi chikomo, koma usamve chisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.
Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,
Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika.
Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.
Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa.
mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna mumtenga akhale mkazi wanu;
Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.
amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.
a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.