Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 11:28 - Buku Lopatulika

Ndipo adzabwerera kudziko lake ndi chuma chambiri; ndi mtima wake udzatsutsana ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake, ndi kubwerera kudziko lake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo adzabwerera kudziko lake ndi chuma chambiri; ndi mtima wake udzatsutsana ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake, ndi kubwerera kudziko lake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mfumu ya kumpoto idzabwerera ku dziko la kwawo ndi chuma chambiri, koma mtima wake udzafunitsitsa pangano lopatulika. Idzawononga panganolo ndipo kenaka idzabwerera ku dziko lake.

Onani mutuwo



Danieli 11:28
7 Mawu Ofanana  

Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano.


Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kuchita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwake kudzakhala pa nthawi yoikika.


Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwera; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.


Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nkugwetsa pansi choonadi, ndi kuchita chifuniro chake, ndipo inakula.


Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo.


Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.