Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.
2 Samueli 9:5 - Buku Lopatulika Pamenepo mfumu Davide anatumiza anthu nakatenga iye kunyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mfumu Davide anatumiza anthu nakatenga iye kunyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo mfumu Davide adatuma anthu kuti akamtenge, ndipo iwo adakamtengadi ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele, ku Lodebara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli. |
Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.
Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara.
Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.