Ndipo kudaipira Davide, chifukwa Yehova anachita chipasulo ndi Uza; natcha malowo Pereziuza, kufikira lero lino.
2 Samueli 6:9 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adachita mantha ndi Chauta tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Chautali lingafike bwanji kwathu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?” |
Ndipo kudaipira Davide, chifukwa Yehova anachita chipasulo ndi Uza; natcha malowo Pereziuza, kufikira lero lino.
Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse.
Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife?