Chomwecho pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri.
2 Samueli 24:9 - Buku Lopatulika Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo m'Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yowabu adapereka chiŵerengero cha anthu onse kwa mfumu. Ku dziko la Israele kunali anthu 800,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kunali 500,000 pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa mfumu: Mu Israeli munali anthu 800,000 amphamvu amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga ndipo mu Yuda munali anthu 500,000. |
Chomwecho pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri.
A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;