Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele.
2 Samueli 2:29 - Buku Lopatulika Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Abinere ndi anthu ake adayenda usiku wonse, nabzola chidikha cha Araba. Adaoloka mtsinje wa Yordani, ndipo adayenda m'maŵa monse, nakafika ku Mahanaimu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usiku wonsewo Abineri ndi ankhondo ake anayenda kudutsa Araba. Iwo anawoloka Yorodani, napitirira mpaka kudutsa dera lonse la Bitironi ndipo anafika ku Mahanaimu. |
Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse.
Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mipata.