Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni.
2 Samueli 2:25 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinere, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa chitunda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinere, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa chitunda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abenjamini adasonkhana pamodzi kuthandiza Abinere, ndipo adapanga gulu limodzi lankhondo, nakaima pamwamba pa phiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anthu a fuko la Benjamini anasonkhana kudzathandiza Abineri. Iwo anapanga gulu ndipo anayima pamwamba pa phiri. |
Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni.
Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?