2 Samueli 2:21 - Buku Lopatulika Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abinere adamuuza kuti, “Patukira mbali ina iliyonse, ukagwire mmodzi mwa ankhondowo, umlande zake.” Koma Asahele sadafune kuti aleke kuthamangitsa Abinere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abineri anati kwa iye, “Khotera kumanja kapena kumanzere: tsatira mmodzi mwa anyamatawa ndipo umulande zida zake.” Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa. |
Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?
Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.