Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire.
2 Samueli 2:15 - Buku Lopatulika Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anyamatawo adabweradi naŵaŵerenga. A fuko la Benjamini, anyamata a Isiboseti, mwana wa Saulo, analipo khumi ndi aŵiri, anyamata a Davide analinso khumi ndi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero anayimirira ndipo anawawerenga: anyamata khumi ndi awiri a fuko la Benjamini ndi Isi-Boseti mwana wa Sauli ndiponso anyamata khumi ndi awiri a Davide. |
Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire.
Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;