Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.
2 Samueli 18:25 - Buku Lopatulika Pamenepo mlondayo anafuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mlondayo anafuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo mlondayo adafuula nauza mfumu. Mfumuyo idati, “Ngati ali yekhayekha, ndiye kuti ali ndi nkhani yabwino.” Tsono munthu uja adafika ndithu, nayandikira pafupi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mlonda uja anapita kwa mfumu ndipo anafotokoza. Mfumu inati, “Ngati ali yekha ali ndi nkhani yabwino” Ndipo munthuyo anayandikira. |
Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.
Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakuchipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, Iyenso abwera ndi mau.