Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.
2 Samueli 17:19 - Buku Lopatulika Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwike. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mkazi wa munthu uja adatenga chivundikiro, nachiika pamwamba pa chitsimecho, nkuyanikapo tirigu, kotero kuti chitsimecho sichinkadziŵika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkazi wake anatenga chophimba ndipo anachiyika pamwamba pa chitsimecho nawazapo tirigu. Palibe amene anadziwa chilichonse za izi. |
Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.
Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mzinda nakweza manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko.