Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
2 Samueli 16:6 - Buku Lopatulika Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali ku dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali ku dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Simeiyo ankaponya miyala mfumu Davide ndiponso nduna zake zonse. Nthaŵiyo nkuti atetezi ake ndi ankhondo ake ali kwete kuzungulira mfumuyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake. |
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.