Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
2 Samueli 14:10 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mfumu idati, “Ngati wina aliyense akunenerani kanthu kena kalikonse, mubwere naye kwa ine, ndipo sadzakuvutitsaninso.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inayankha kuti, “Ngati wina aliyense anene kanthu kwa iwe, umubweretse kwa ine, ndipo sadzakuvutitsanso.” |
Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wachifumu wao zikhale zopanda chifukwa.
Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.