Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
2 Samueli 13:35 - Buku Lopatulika Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana aamuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana amuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva zimenezi Yonadabu adauza mfumu kuti, “Ana a mfumu abwera. Amfumu, monga momwe ndinakuuzirani muja, ndi m'mene zayendera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.” |
Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana aamuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.