Ndipo anyamata a Abisalomu anamchitira Aminoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana aamuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yake, nathawa.
2 Samueli 13:30 - Buku Lopatulika Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana aamuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana amuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthuwo akali m'njira, Davide adamva mphekesera zakuti Abisalomu wapha ana onse aamuna a mfumu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsalako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.” |
Ndipo anyamata a Abisalomu anamchitira Aminoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana aamuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yake, nathawa.
Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong'ambika.
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.