Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.
2 Samueli 13:10 - Buku Lopatulika Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aminoni adauza Tamara kuti, “Bwera nacho chakudya chija m'chipinda muno kuti ndidzadyere m'manja mwako.” Tamara adatenga makeke amene adaaphikawo, napita nawo kwa Aminoni, mbale wake, m'chipindamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake. |
Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.
Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.