Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwere kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikire kunyumba yako?
2 Samueli 11:9 - Buku Lopatulika Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Uriya adagona pakhomo pa nyumba ya mfumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake, sadapite kunyumba kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake. |
Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwere kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikire kunyumba yako?
Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake.
Ndipo mfumu Rehobowamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.
Ndipo kunachitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku chipinda cha olindirirawo.