2 Samueli 11:23 - Buku Lopatulika Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatipambana natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatilaka natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. |
Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.