Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.
Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo polowera kuchipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.